Pitilizani kuthandiza FLA – Ntelera
Mkulu woyendetsa ntchito yosaka ndalama zoyendetsera bungwe la Football Legends Association (FLA) a Rashid Ntelera ayamikira anthu osiyanasiyana omwe akuthandiza bungweli kuyendetsa ntchito zake m’dziko muno.
Ntelera walakhula izi pomwe FLA lalengeza kuti ma Jersey a ma Legends akhala akuyambiranso kupezeka pa msika kuyambira pa 29 March chaka chino, ponena kuti ma Jersey 2,500 ndi omwe agulidwa kuchokera ku South Africa.
Malinga ndi Ntelera, mtengo wagulira ndi K55,000, ndipo ndalama zake zimanthandizira kuyendetsa ntchito za bungwe li.
Iye wati mwanzina FLA likupitiriza kulipira mgwirizano woti osewera mpira wamiyendo akalewa azipeza thandizo la chipatalala, pakutsatira kwa mgwirizano omwe adapanga ndi kampani ya MedHeath mwezi wa January.
Ntelera wapempha anthu okonda masewero ampira wamiyendo komaso akufuna kwabwino kugwirana manja ndi bungweli pogula katundu yu,ngati njira imodzi yopititsa patsogolo umoyo ndi chisamaliro cha osewera akake.
Pakadalipano osewera akale okwana 55 ndi omwe akulandira nawo thandizo lamakhwala muzipatala zosiyanasiyana mwa ulele.
Bungwe la Football Legends Association (FLA) limatsogozedwa ndi a Jim Kalua, ndipo zina mwa zolinga zake ndikupititsa patsogolo chisamaliro cha osewera akale.
The post Pitilizani kuthandiza FLA – Ntelera appeared first on Malawi Voice.